Malawi Observer

Alipire chindapusa cha K5.5 million Kaamba koluma ndi kudula phuno ya membala wa MCP

Bwalo la milandu la Kasungu lalamula m’modzi mwa otsogolera achinyamata ku chipani cha UTM mchigawo chapakati, a Alick Saini kuti apereke K5,050,000 ngati chindapusa kaamba koluma ndikudula mphuno ya Chisomo Kefa, mtsogoleri wa achinyama a MCP.

A Saini adapalamula mlanduwu pa 1 September chaka chino atasemphana chichewa ndi a Kefa pa nkhani za pa chiweniweni.

Mwa ndalamazi K4.5 miliyoni ndi chipukuta misonzi chopitsa kwa Kefa pomwe K550,000 ndi yopita ku boma.

Asaini akuyenera kupereka K1.5 miliyoni kwa a Kefa komanso K550,000 ku boma lero kuti awamasule ndipo ndalama yotsalayo awapatsa miyezi isanu kuti amalize.

Magistrate Jones Masula wabwaloli wati wapereka chilangochi chifukwa zomwe adachita a Saini zidapereka chilema chamuyaya kwa a Kefa.

Exit mobile version