Thursday, December 26, 2024
الرئيسيةLatestChipani cha PDP chizayima pachokha

Chipani cha PDP chizayima pachokha

Chipani cha Peoples Development (PDP) chidzatenga gawo pa chisankho cha 2025, poyima paokha.

Mtsogoleri wa chipanichi a Kondwani Nankhumwa anena izi pa msonkhano waukulu wa chipanichi ku Blantyre.

M’mawu awo ati anthu ena akhala akuganiza kuti chipani cha PDP chilibe chikoka kumadera a mdziko muno koma lero azionela okha.

Iwo ati kudzera pa msonkhanowu pomwe pabwera nthumwi zochokera maboma onse mdziko lino, ndichitsimikizo kuti chipanichi ndichamphamvu choncho sakuganiza kuti ndikoyenera kugwirizana ndi zipani zina.

Mthumwi pa msonkhano wu zatsimikiza kuti a Nankhumwa ndiwo mtsogoleri wachipanichi kwa zaka zisanu zikubwerazi ndipo iwo adutsa popanda opikisana naye.

Nthumwizi zasankhanso a Rose Sagala kukhala wachiwiri kwa mtsogoleri wachipanichi pomwe a Semion Phiri ndiwo awasankha kukhala mlembi wamkulu wachipanichi.

مقالات ذات صلة

ترك الرد

من فضلك ادخل تعليقك
من فضلك ادخل اسمك هنا

- Advertisment -
Google search engine

الأكثر شهرة

احدث التعليقات