Thursday, December 26, 2024
الرئيسيةLatestKhoti litumiza a Billy Malata ku ndende ya Maula poipitsa mbiri ya...

Khoti litumiza a Billy Malata ku ndende ya Maula poipitsa mbiri ya a ena pogwiritsa ntchito masamba a mchezo

Bwalo la milandu laling’ono ku Nathenje, latumiza mkulu woyang’anira nkhani za ndale m’chipani cha DPP, a Fredrick Billy Malata ku ndende ya Maula kwa masiku asanu ndi awiri (7).

A Malata, adamangidwa loweruka pa mlandu woipitsa mbiri ya wochita malonda a Alfred Gangata pogwiritsa ntchito masamba a mchezo.

Iwo adatengeredwa ku bwalo la milandu ku Nathenje dzulo ndipo bwalo lawatumiza ku Maula kwa amasiku 7 ponena kuti chigamulo pa pempho lawo la belo chidzapelekedwa Lachiwiri sabata ya mawa.

Owayimilira a Malata a Gladwell Majekete atsimikiza za izi ndipo ati a Malata akasiyidwa ku Maula m’mawa wa lero atagona usiku wadzulo ku polisi ya Nathenje.

Akulowa ku ndende ya Maula, a Malata adalankhura mwachidule ndi Times 360 Malawi ndipo anati: “Amalawi akufuna kwabwino andithandize. Ombudsman, a Chief Justice komanso Inspector General of police andithandize ndikuvutika. Ndagona ku Area 3 police masiku atatu, dzulo ndagona ku Nathenje lero akukandisiya ku Maula pa nkhani zosamveka. Panopa mu zovala zanga muli msikidzi zokhazokha, ndikuvutika.”

مقالات ذات صلة

ترك الرد

من فضلك ادخل تعليقك
من فضلك ادخل اسمك هنا

- Advertisment -
Google search engine

الأكثر شهرة

احدث التعليقات